KUPANGA INSTALL WINDOWS MU COMPUTER KUGWIRITSA NTCHITO USB FLASH DISK GAWO LOYAMBA - PART 1
Kupanga install windows ndi chimodzi mw ukadaulo umene munthu aliyese yemwe amakonza ma computer amayenera kudziwa. ngati inu muli mmodzi mwa okonza kapena mukuna mutaphunzira kuti muzipanga install windows panoka, sangalalani ndipo khalani tcheru chifukwa lero tikhala tikutambasula ndondomeko zoyenera kutsata popanga install windows.
Lero tiuzana za mmene tingapangire install windows mu computer iliyonse posatenger kuti ndi laptop kapena dektop. Tigwiritsa ntchito Windows 7 pofuna kupanga instsall windows. Ndondomeko yopanga install Windows siimasiyana kwenikweni ndipo ngati mungakwaitse kupaga install windows 7 pakutha pa ndndomeko imene tikukambirana apayi, sikungakhalenso kovuta kupanganso install windows 7,8 ,8.1,10 komanso windows 11.
Zoyenera kudziwa:
Ndondomeko iyi ikupanga ikukuikani pa mlingo mukupanga install windows koyamba kapena kupanga install windows kumakuvutani, chotero sitikamba zambiri mwatsatane pakadali pano. Mukafuna kumvetsetsa zambiri zokhudzana ndi kupanga install windows khalani tcheru pa forum pano.
Windows aliyense ali Muchizungu ndiye mukamapanga install Windows mukuyenera kukhala omvetsetsa zina mwa zomwe malangizo/instructions kapna ndondomeko/procesures ya Windows ikunena poopa kufufuta zinthu zofunikira mu Harddrive
Zofunika
Kuti tipange install windows tikuyenera kukhala ndi zinthu izi
- USB flash disk/Memory Card yosachepera 8GB
- Windows ISO Image - pangani download Windows 7
- Rufus - pangani download rufus
Ngati zinthu zonse zatchulidwa muli nazo kale tiyeni chitsogolo.
Kuika windows mu flash/ kupanga bootable flash
Tsekulani Rufus (rufus.exe) , ikani USB Flash Drive ndipo ndipo ngati flash yapangidwa detect ndi rufus, muone pansi pomwe alemba Device pabwera Dzina la flash (drive letter:)[Size]. Mwachitsanzo itha kulemba chochi ; New volume (E:) [16GB].
Pitani pansi pa Boot selection kenako sankhani button yolembedwa "SELECT" kenako lozerani komwe mwasunga windows image yanu ija,
mukamupeza musankheni mpaka mutaona dzina la image yomwe mwasankha ija litabwera kumazele kwa button "SELECT". Ngati mwasankha windows 7 pitirirani pansi penipeni pomwe alemba start ndipo mutobwanye pamenepo. Ngati mukupanga za windows 8 kepena kupita mmwamba sinthani pomwe alemba partition scheme ikhale MBR ndipo pitani pomwe pelmbedwa start.
Chenjezo: Kupirira ndi ndodndomeko yopanga bootable USB flash zimafufuta zinthu zonse za mu flash ndiye ngati mu Flash yomwe ikugwiritsidwa ntchito muli zinthu zofunikira, zisungeni kaye.